top of page

COKANI MUMDIMA, LONDOLANI KUUNIKA

Kodi Mulungu afuna kuti ticite bwanji ndi ziwanda?

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu – Yakobo 4.7

 

Kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuka kucokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kucokera ulamulirao wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo cikhululukiro ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi cikhulupiriro ca mwa Ine – Macitidwe 26.18

 

Tingoyerekeze kuti ndi usiku. Muli ciimirire pabwalo pofuna kupita kunyumba. Kwada kwambiri. Kuli zii. Mumdima ndi cosabvuta kumva kuti ndinu nokha, osatetezeka ndi amantha. Kodi ngati ndinu muli pabwalo mumdima woopsetsa, mungacite ciani? Mwina ambiri a ife angapemphere. Mwina ena angathamange kuti afike kunyumba mwamsanga. Ena angayende pang’ono-pang’ono, okhala tcheru ku cipsezo cobisika.

Nthawi zambiri tikumva kuti palibe ciriconse cimene tingacite kuti tipulumuke mdima. Tingofuna kuti sikudzakhala ngozi. Komabe kuli cinthu cimodzi cokwanitsa kuthamangitsa mdima: kuunika.  Mdima sungapirire kuwala. Kukakhala kuwala, mdima umatha. Ici ndi cimodzimodzi mu zauzimu: mdima (Satana ndi ziwanda) sungakhalepo pali kuunika (Mulungu).

Yesu ndi Kuunika kwa dziko lapansi. Tembenukirani kwa Iye.

 

Satana ndiye mdani wa Mulungu

Baibulo litiuza kuti Mulungu analenga zonse[1]. Analenga angelo kumwamba naonso[2]. Zonse zolengedwa ndi Mulungu zinali bwino[3]. Komabe tsiku lina mngelo mmodzi anaukira Mulungu[4]. Mngeloyo wocimwa anatumizidwa kutali pamodzi ndi omutsatira[5]. Mngeloyo wocimwa ndi wochedwa Satana kapena mdierekezi. Ndipo angelo ena onse olondola Satana ndi ochedwa ziwanda.

Mulungu ndi Satana ndi osiyana kwambiri.

Mulungu ndi coonadi[6]. Satana ndi tate wa bodza[7].

Mulungu ndi wamphamvuyonse[8]. Satana ndi wocepa mphamvu[9].

Mulungu ndi cikondi[10]. Satana adana ndi Mulungu ndi anthu.

Mulungu ndi woyera ndi wolungama[11]. Satana ndi wocimwa[12].

Mulungu ali ponseponse nthawi imodzi[13]. Satana ali ndi malire[14].

Mulungu ndi wokhulupirika[15]. Satana ndi wonyenga[16].

Mulungu abweretsa mtendere[17]. Satana abweretsa msokonezo[18].

Mulungu ndi wacifundo[19]. Satana ndi wankhanza[20].

Mulungu apereka moyo[21]. Satana aononga[22].

 

Yesu ndi Kuunika kwa dziko lapansi. Tembenukirani kwa Iye.

 

Satana, ziwanda ndi anthu

Satana ndi ziwanda atathamangitsidwa kumwamba, anafuna kubwezera Mulungu moononga cilengedwa ca Mulungu.

Mobisa Satana anayesa Adamu ndi Hava, ndiwo anthu oyamba padziko lapansi, kuti asamvere Mulungu. Adamu ndi Hava anamvera Satana. Anacimwira Mulungu: iwonso anapandukira Mulungu[23]. Kuyambira pamenepo aliyense ali pansi pa ulamuliro wa Satana mwa cibadwire[24]. Citanthauza kuti aliyense ali ndi cilakolako cobadwa naco cofuna kudzikondweretsa iye mwini osati Mulungu.

Satana ndi ziwanda amayesa kuti tikopedwe m’njira ziwiri:

  1. Atiyesa kucimwa ndipo tibvomera[25]. Mwacitsanzo, ngati munthu wina ataya ndalama za m’thumba mwake, tingayesedwe kuti tisakambepo koma kungodoba ndalamazo ndi kuzisewenzetsa. Kapena ngati wina atipatsa ndalama zoti tigone ndi mwamuna kapena mkazi kunja ku ukwati, Satana angatiuze kuti si chimo. Angatiuze kuti ndi njira yothandiza mabanja athu kuwagulira zosowa zao.

  2. Tiyambitsa chimo, ziwanda zibvomera ndi kutilimbikitsa[26]. Mwacitsanzo, tikafuna kudziwa cifukwa ca bvuto lina la m’moyo, tingapite ku African doctor. Satana adzaonetsetsa kuti tidzapeza thandizo. Motero tiganiza kuti kuombeza si chimo. Kapena ngati tikumva osasamalidwa m’ukwati, tingalake kupeza mwamuna kapena mkazi wina. Satana angabweretse anthu panjira pathu otipatsa cisamaliro capadera kuti potsiriza pake ticite cigololo.

Satana sadziwa maganizo athu koma akhoza kutiyang'ana, kutilimbikitsa, ndi kutinong'oneza m'maganizo mwathu[27].

Yesu ndi Kuunika kwa dziko lapansi. Tembenukirani kwa Iye.

 

Yesu ndiye Kuunika

Mulungu ndi Kuunika[28]. Ndipo Yesu mwana wa Mulungu, anati kuti Iye ndiye Kuunika:

Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo – Yohane 8.12

Pamene Yesu anafa pamtanda, anagonjetsa Satana kwamuyayaya[29]. Yesu ndi yankho lokha la mdima. Tidzifunse ngati tidziwadi, kubvomera ndi kumvera Yesu monga Mpulumutsi ndi Mbuye.

Ngati tikalibe kulapa macimo athu, tikhalabe mumdima[30]. Tili pansi pa ulamuliro wa Satana. Tilibe citetezo ku ziwanda. Njira yokhayo yothawira mumdima ndiyo kulapa ndi kukhulupirira Yesu.

Ngati ndife anthu olapa ndi okhulupirira Yesu ku cipulumutso ca macimo athu ndife otsatira a Yesu Kuunika[31]. Tamasulidwa ku mdima[32]. Sitiyenera kuopa mphamvu zoipa. Ndife otetezedwa ndi Mulungu[33]. Tiyenera kupewa macimo (ndiwo mdima)[34].

Yesu ndi Kuunika kwa dziko lapansi. Tembenukirani kwa Iye.

 

Kodi tingathawe bwanji Satana?

Ngakhale Satana ndi wogonjetsedwa, ayesetsabe kutikokera kutali ndi Mulungu. Tizimukaniza mwa kubvala zida za Mulungu[35]:

  • Dziwani ndi kugwira molimbika coonadi[36]. Werengani, dziwani Baibulo. Mvetsetsani citanthauzo ca kukhala opulumutsidwa ndi Yesu.

  • Khalani okonzeka kumvera Mulungu[37]. Osapotoza Baibulo. Ena anena kuti nzeru za ang’anga ena ndi zabwino zicokera kwa Mulungu. Ici ndi bodza. Mulungu adana ndi miyambo yotere[38]. Sankhani zoyenera.

  • Khulupirirani Mulungu[39]. Tingayesedwe kuganiza kuti Mulungu yekha ndi wosakwanira kutithandiza ndi kutiteteza. Ici ndi bodza. Tiyenera kukhala ndi cikhulupiriro mwa Mulungu kuti tidzitetezere kuti tisagonje ndi mayesero.

  • Dalirani coonadi ca Mulungu. Tiziika ciyembekezo cathu mwa Mulungu. Osataya ciyembekezo pa ciriconse. Mulungu alamulira[40]. Angalole zoipa zicitike pa colinga[41]. Osakayikira ubwino wake.

  • Pempherani kosaleka[42]. Mulungu atipatsa nzeru ndi mphamvu kuti tikane mdierekezi. Tiyenera kudalira pa Iye kwathunthu.

 

Zotsatira zake zenizeni

  • Osacita chidwi pa nkhani za Satana ndi ziwanda[43]Satana ndi ziwanda akondwa ngati tiganizira ndi kulankhula za iwo. Sadandaula ngati ticita misonkhano yotulutsa ziwanda koma adandaula ngati anthu alapa ndi kukhulupirira Yesu pa cipulumutso. Musalemekeze ziwanda mwa kuononga ndalama kapena nthawi pa ciriconse cokhudzana nazo.

  • Anthu ogwidwa ndi ziwanda, afunika kudziwa Yesu[44]Anthu ayenera kumvetsetsa Uthenga Wabwino wa Yesu Kuunika ndi kudzipereka kwa Iye mwathunthu. Ayenera kuphunzitsidwa Baibulo ndi kupemphereredwa[45]. Sitifunikira opemphera apadera kuti titero[46]. Sitilamulidwa kutulutsa ziwanda. Mulungu adzathana ndi ziwanda mwa ciphunzitso ca m'Baibulo ndi pemphero. Kumbukirani kuti Baibulo limacha ambiri oturutsa ziwanda, akucita kusayeruzika[47].

  • Osapatsa Satana ndi ziwanda malo m'maganizo mwanu[48]. Cinthu coipa cikacitika, nthawi zambiri tiganiza kuti mzimu woipa wacilengetsa. Maganizo amenewa asonyeza kuti mizimu yoipa ili ndi malo m'maganizo mwathu. M'malo mwake, maganizo athu ayenera kudzazidwa ndi Mulungu[49].

  • Dziwani Mulungu bwino kwambiri mwa BaibuloTikadziwa Mulungu mwa Baibulo, tidzakhoza kuika poyera mabodza a Satana. Baibulo linena kuti:

    • Mizimu ya akufa sionekera kwa anthu amoyo[50]. Palibe cifukwa cocitira mwambo woti tidziteteze kapena kuteteza makanda kuti mizimu ya akufa singatiyendere.

    • Makolo athu anatisiyira nzeru yacabe ndi yoipa[51]. Nthawi zonse yesani ngati zomwe makolo athu anatiuza zigwirizana ndi Baibulo. Baibulo lokha ndi coonadi.

    • Kulibe mizimu yosiyana ya macimo amitundu yonse[52]. Anthu ocimwa safunika kumasulidwa ku ciwanda cina cake. M'malo mwake Baibulo liwauza kuti alape ndi kukhulupirira Yesu[53].

  • Osaopa ngati muli mwa Yesu. ‘Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirani kuletsa woipayo’ (2 Atesalonika 3.3).

 

Kuti asaticenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa macenjerero ace – 2 Akorinto 2.11

--------------------------------------------------

[1] Genesis 1 ndi 2, [2] Akolose 1.16, [3] Genesis 1.31, [4] Yuda 1.6, [5] Cibvumbulutso 12.7-9, [6] Masalmo 31.5, [7] Yohane 8.44, [8] Luka 1.37, [9] 1 Yohane 4.4, [10] 1 Yohane 4.16, [11] Yesaya 6.3, Masalmo 11.7, [12] 1 Yohane 3.5, [13] Yeremiya 23.24, [14] Yobu 1.7, Yobu 2.6, [15] Maliro 3.23, [16] Genesis 3.1-4, [17] Yohane 14.27, 1 Corinthians 14.33, [18] Cibvumbulutso 12.9, [19] Eksodo 34.6, [20] Yohane 10.10, [21] Yohane 10.10, [22] 1 Petro 5.8, [23] Genesis 3, [24] Aroma 5.19, Aroma 5.12, Aefeso 2.2-3, [25] 1 Petro 5.8, Aroma 6.16, Luka 22.31, [26] Yakobo 1.14, 2 Akorinto 11.14, [27] 2 Akorinto 11.3, Yobu 1.7, Yohane 13.2, [28] 1 Yohane 1.5, [29] Akolose 2.15, 1 Yohane 3.8, [30] Aefeso 4.18, Yohane 3.19-20, Aefeso 2.2-3, [31] Yohane 8.12, [32] Akolose 1.13-14, Aefeso 5.8, [33] 2 Atesalonika 3.3, [34] 1 Yohane 1.5-6, [35] Aefeso 6.10-18, [36] 2 Timoteo 1.13, Afilipi 2.16, [37] Yakobo 1.22, Yohane 14.15, [38] Deuteronomo 18.10-12, Agalatiya 5.19-21, Cibvumbulutso 21.8, [39] Masalmo 62.5-6, 2 Akorinto 12.9, [40] Aefeso 1.11, Mateyu 10.29-30, Miyambi 3.5-6, Miyambi 16.9, [41] Aroma 8.28, [42] Akolose 4.2, 1 Atesalonika 5.17, 1 Yohane 4.4, [43] Yakobo 4.7, [44] Luka 4.18-19, 1 Yohane 4.4, [45] Masalmo 119.105, [46] 1 Timoteo 2.5, [47] Mateyu 7.21-23, [48] Aefeso 4.27, [49] Afilipi 4.8, Akolose 3.2, [50] Mlaliki 9.5-6, Yobu 7.9-10, [51] 1 Petro 1.18-19, [52] Yakobo 1.14, Marko 7.21-23, Agalatiya 5.19-21, [53] 1 Yohane 1.9, Macitidwe 3.19

  • YouTube

Kulembanso zinthu ndi colinga copangirapo ndalama sikuloledwa.

©2026 Stephanos Zambia Trust

Mfundo yosunga zisinsi

bottom of page